Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 55:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+

  • Ezekieli 33:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Auze kuti, ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa,+ koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere+ kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.+ Bwererani! Bwererani ndi kusiya njira zanu zoipa.+ Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?”’+

  • Habakuku 1:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo n’chifukwa chiyani pali mikangano ndi kumenyana?+

  • Habakuku 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Inu ndinu woyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa ndipo simungathe kuonerera khalidwe loipa.+ N’chifukwa chiyani mumayang’ana anthu amene amachita zachinyengo,+ ndipo n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala chete pamene munthu woipa akumeza munthu amene ndi wolungama kuposa iyeyo?+

  • Aroma 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+

  • Aroma 9:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Bwanji ngati Mulungu analekerera moleza mtima kwambiri ziwiya za mkwiyo zoyenera kuwonongedwa ngakhale kuti akufuna kuonetsa mkwiyo wake ndi mphamvu zake?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena