Yobu 14:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda,+Mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utachoka,Mukanati mundiikire nthawi+ n’kudzandikumbukira.+ Yobu 17:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndidzaitana dzenje+ kuti, ‘Ndinu bambo anga!’Kwa mphutsi+ ndidzati, ‘Mayi anga ndi mlongo wanga!’ Yesaya 38:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 M’malo mopeza mtendere ndinapeza zowawa, zowawatu zedi!+Inuyo mwamamatira moyo wanga ndipo mwauteteza kuti usapite kudzenje la chiwonongeko.+Pakuti machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.+ Machitidwe 13:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Ndipo mu salimo lina akunenanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.’+
13 Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda,+Mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utachoka,Mukanati mundiikire nthawi+ n’kudzandikumbukira.+
17 M’malo mopeza mtendere ndinapeza zowawa, zowawatu zedi!+Inuyo mwamamatira moyo wanga ndipo mwauteteza kuti usapite kudzenje la chiwonongeko.+Pakuti machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.+