Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 25:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Chotero Aisiraeli anayamba kupembedza nawo Baala wa ku Peori.+ Pamenepo, mkwiyo wa Yehova unawayakira.+

  • Numeri 31:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kodi mwaiwala kuti akaziwa ndi amene anatsatira mawu a Balamu? Si ndiwo kodi amene ananyengerera ana a Isiraeli kuti achimwire Yehova pa zochitika za ku Peori,+ kuti mliri ugwere khamu la anthu a Yehova?+

  • Deuteronomo 4:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita pa nkhani ya Baala wa ku Peori, kuti munthu aliyense amene anatsatira Baala wa ku Peori,+ Yehova Mulungu wanu anamuwononga ndi kum’chotsa pakati panu.+

  • Deuteronomo 32:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Iwo anali kupereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+

      Anapereka nsembe kwa milungu imene sanaidziwe,+

      Milungu yatsopano yongobwera kumene,+

      Imene makolo anu akale sanaidziwe.

  • Hoseya 9:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zam’chipululu.+ Ndinaona makolo a anthu inu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu wongoyamba kumene kubereka.+ Iwo anapita kwa Baala wa ku Peori+ ndipo anadzipereka kwa chinthu chochititsa manyazicho.+ Anakhala onyansa ngati chinthu chimene anali kuchikondacho.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena