-
1 Samueli 24:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Tsopano, bambo anga,+ onani. Taonani kansalu ka m’munsi mwa malaya anu akunja odula manja. Pakuti mmene ndinali kudula kansalu kameneka sindinakupheni. Ndiyetu dziwani ndi kuona kuti ndilibe maganizo oipa+ kapena oukira, ndipo sindinakuchimwireni, ngakhale kuti inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe.+
-
-
2 Akorinto 1:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ifeyo tili ndi chifukwa chodzitamandira chakuti m’dzikoli, makamaka pakati pa inuyo, tachita zinthu zoyera ndiponso moona mtima mogwirizana ndi zimene Mulungu amaphunzitsa. Tachita zimenezi osati modalira nzeru+ za m’dzikoli koma modalira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndipo chikumbumtima chathu chikuchitiranso umboni zimenezi.+
-