Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 13:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Uwu ndi uthenga wokhudza Babulo,+ umene Yesaya mwana wa Amozi+ anaona m’masomphenya:

  • Yesaya 47:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 47 Tsika ukhale pansi pafumbi+ iwe namwali, mwana wamkazi wa Babulo.+ Khala padothi pomwe palibe mpando wachifumu,+ iwe mwana wamkazi wa Akasidi.+ Pakuti anthu adzaleka kukutchula kuti ndiwe wolekereredwa ndiponso wosasatitsidwa.*+

  • Yeremiya 25:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwanira,+ ndidzabwezera mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo zolakwa zawo.+ Ndidzabwezera zolakwa za dziko la Akasidi+ ndipo dziko lawolo lidzakhala mabwinja mpaka kalekale,’+ watero Yehova.

  • Yeremiya 50:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Nenani ndi kulengeza zimene zachitika kwa anthu a mitundu ina.+ Imikani mtengo wachizindikiro+ ndipo lengezani zimenezi. Musabise kalikonse amuna inu. Nenani kuti, ‘Babulo walandidwa.+ Beli wachititsidwa manyazi.+ Merodake wachita mantha. Mafano a Babulo achita manyazi.+ Mafano ake onyansawo* achita mantha.’

  • Chivumbulutso 18:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu,+ akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya+ uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonse yonyansa ndi yodedwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena