29 Choncho Mose anamuyankha kuti: “Ndikangotuluka mumzinda uno, ndikweza manja anga kwa Yehova.+ Mabingu ndi matalala asiya, kuti mudziwe kuti dziko lapansi ndi la Yehova.+
11 Inu Yehova, ukulu,+ mphamvu,+ kukongola,+ ulemerero,+ ndi ulemu+ ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi ndi zanu.+ Ufumu+ ndi wanu, inu Yehova, ndinunso Wokwezeka monga mutu pa onse.+