Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 6:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 mboni yachinyengo yonena mabodza,+ ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.+

  • Miyambo 20:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Woyenda uku ndi uku n’kumanena zoipa za anthu ena amaulula zinsinsi,+ ndipo usamagwirizane ndi munthu wotengeka ndi milomo yake.+

  • Yohane 8:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi,+ ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu.+ Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake,+ ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.+

  • Akolose 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Musamanamizane.+ Vulani umunthu+ wakale pamodzi ndi ntchito zake,

  • 1 Timoteyo 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nawonso amayi akhale opanda chibwana, osati amiseche.+ Akhale ochita zinthu mosapitirira malire,+ ndi okhulupirika m’zinthu zonse.+

  • Chivumbulutso 21:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa,+ opha anthu,+ adama,+ ochita zamizimu, opembedza mafano,+ ndi onse abodza,+ gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto+ ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+

  • Chivumbulutso 22:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu,+ amene amachita zamizimu,+ adama,+ opha anthu, opembedza mafano, ndi aliyense wokonda kulankhula ndi kuchita zachinyengo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena