Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 20:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kenako Abulahamu anayamba kum’pempherera iye kwa Mulungu woona.+ Chotero Mulungu anachiritsa Abimeleki ndi mkazi wake, ndi akapolo ake aakazi, moti iwo anayamba kubereka ana.

  • Ekisodo 15:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndiyeno anawauza kuti: “Ngati mudzamveradi mawu a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani miliri iliyonse imene ndinagwetsera Iguputo,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikukuchiritsani.”+

  • 2 Mafumu 20:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Bwerera, kauze Hezekiya mtsogoleri+ wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu+ wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva+ pemphero lako,+ ndipo ndaona misozi yako.+ Ndikuchiritsa.+ Pa tsiku lachitatu udzapita kunyumba ya Yehova.+

  • Salimo 6:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Ndikomereni mtima, inu Yehova, chifukwa ndikulefuka.+

      Ndichiritseni,+ inu Yehova, chifukwa mafupa anga agwedezeka.

  • Salimo 103:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Tamanda amene akukukhululukira zolakwa zako zonse,+

      Iye amene akukuchiritsa matenda ako onse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena