Salimo 37:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+ Salimo 112:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+ צ [Tsa·dhehʹ]Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ק [Qohph]Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+ Luka 6:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Aliyense amene wakupempha kanthu mupatse,+ ndipo amene wakulanda zinthu usamuumirize kuti abweze. 2 Akorinto 8:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pakuti mukudziwa kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti ngakhale kuti iye anali wolemera, anakhala wosauka chifukwa cha inu,+ kuti inuyo mulemere+ kudzera m’kusauka kwake.
9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu aumphawi.+ צ [Tsa·dhehʹ]Chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.+ ק [Qohph]Nyanga* yake idzakwezedwa ndi ulemerero.+
9 Pakuti mukudziwa kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti ngakhale kuti iye anali wolemera, anakhala wosauka chifukwa cha inu,+ kuti inuyo mulemere+ kudzera m’kusauka kwake.