Mlaliki 2:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Ineyo ndinaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse.+ Nditatero, ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe ndipo kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+ Yesaya 55:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 N’chifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya, ndipo n’chifukwa chiyani mukuvutika kugwirira ntchito zinthu zimene sizikhutitsa?+ Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino,+ ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.+ Mateyu 16:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?+ Kapena munthu angapereke chiyani chosinthanitsa+ ndi moyo wake? Yohane 6:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka,+ koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha,+ chimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate, Mulungu yekhayo, waika chisindikizo pa iye chomuvomereza.”+
11 Ineyo ndinaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse.+ Nditatero, ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe ndipo kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+
2 N’chifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya, ndipo n’chifukwa chiyani mukuvutika kugwirira ntchito zinthu zimene sizikhutitsa?+ Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino,+ ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.+
26 Kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?+ Kapena munthu angapereke chiyani chosinthanitsa+ ndi moyo wake?
27 Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka,+ koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha,+ chimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate, Mulungu yekhayo, waika chisindikizo pa iye chomuvomereza.”+