Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 27:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Chotero zolakwa za Yakobo zidzaphimbidwa mwa njira imeneyi.+ Zimenezi zidzachitika akadzachotsa tchimo lakelo,+ ndiponso akadzasandutsa miyala yonse ya paguwa lansembe kukhala miyala yofewa kwambiri yonyenyekanyenyeka, moti mizati yopatulika+ ndi maguwa ofukizirapo zonunkhira sizidzamangidwanso.+

  • Ezekieli 36:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ine ndidzakuwazani madzi oyera ndipo mudzakhala oyera. Ndidzakuyeretsani+ pokuchotserani zonyansa zanu zonse+ ndi mafano anu onse onyansa.+

  • Ezekieli 37:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Iwo sadzadziipitsanso ndi mafano awo onyansa, zinthu zawo zonyansa ndi zochita zawo zonse zophwanya malamulo.+ Ndidzawapulumutsa ku machimo onse amene anali kuchita m’malo awo okhala, ndipo ndidzawayeretsa.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+

  • Hoseya 14:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Efuraimu adzanena kuti, ‘Kodi mafano ndi a chiyaninso kwa ine?’+

      “Ine ndidzamva ndipo ndidzapitirizabe kumuyang’anira.+ Ine ndili ngati mtengo waukulu wa mkungudza wamasamba obiriwira+ ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.”

  • Zekariya 13:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova wa makamu wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathetsa mayina a mafano m’dziko lonseli+ ndipo mafanowo sadzakumbukiridwanso. M’dzikoli ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena