20 M’tsiku limenelo, otsala a Isiraeli+ ndi opulumuka a nyumba ya Yakobo sadzadaliranso yemwe akuwamenya,+ koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova, Woyera wa Isiraeli.+
5 “Pakuti Mulungu, Yehova wa makamu,+ sanasiye Isiraeli ndi Yuda+ kuti akhale mkazi wamasiye. Dziko la Akasidi lili ndi mlandu waukulu pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+