17 ‘Ndithudi, maso ako ndi mtima wako sizikulakalaka china chilichonse koma phindu lachinyengo,+ anthu osalakwa kuti ukhetse magazi awo+ komanso kuba mwachinyengo ndi kulanda.’
2 Iwo alakalaka minda ya anthu ena ndipo ailanda.+ Alakalakanso nyumba za anthu ena n’kuzitenga kukhala zawo.+ Atenga mwachinyengo cholowa cha munthu ndi cha banja lake.+
9 “‘Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo.+ Iye akuchita zimenezi kuti amange chisa chake pamalo okwezeka ndi cholinga choti tsoka lisamupeze.+