19 Anthu a ku Ziyoni+ akadzabwerera n’kukakhala ku Yerusalemu,+ iwe sudzaliranso.+ Mosakayikira, iye adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako. Akadzangomva kulira kwakoko, iye adzakuyankha.+
10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+