8 Msuri adzaphedwa ndi lupanga, koma osati la munthu. Lupanga lidzamudya, koma osati la munthu wochokera kufumbi.+ Iye adzathawa chifukwa cha lupangalo ndipo ana ake aamuna adzagwiritsidwa ntchito yaukapolo.
3 Wafanana ndi Msuri. Wafanana ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,+ wanthambi zikuluzikulu zokongola,+ wanthambi za masamba ambiri zopereka mthunzi, mtengo wautali kwambiri+ umene nsonga yake inafika m’mitambo.+