Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 15:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kuchokera pamenepo, anapitirira mpaka kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ kumalo otsetsereka otchedwa Yebusi+ kum’mwera, kutanthauza Yerusalemu.+ Anapitirirabe mpaka pamwamba pa phiri loyang’anizana ndi chigwa cha Hinomu, limene lili kumadzulo kwa chigwacho. Phirilo lili kumpoto kwa chigwa cha Arefai,+ kumapeto kwa chigwacho.

  • 2 Mafumu 23:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mfumuyo inachititsa kuti ku Tofeti,+ m’chigwa cha ana a Hinomu+ kukhale kosayenera kulambirako, kuti munthu aliyense asawotcheko* mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi pamoto,+ pomupereka kwa Moleki.+

  • 2 Mbiri 28:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ahazi anafukiza nsembe yautsi+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Iye anawotcha ana ake+ pamoto mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+

  • Yeremiya 7:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Iwo amanga malo okwezeka ku Tofeti,+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ kuti azitentha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuchita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena