Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 12:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Usapembedze Yehova Mulungu wako m’njira imeneyi,+ pakuti iwo amachitira milungu yawo zonse zimene zili zonyansa kwa Yehova, zimene iye amadana nazo. Pakuti iwo nthawi zonse amatentha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto monga nsembe kwa milungu yawo.+

  • 2 Mafumu 17:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Iwo anapitiriza kuwotcha* pamoto+ ana awo aamuna ndi aakazi, kulosera+ ndi kuwombeza.*+ Anapitirizanso+ kuchita zoipa* pamaso pa Yehova ndi cholinga chomukwiyitsa.+

  • Salimo 106:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Anali kupereka nsembe ana awo aamuna+

      Ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.+

  • Salimo 106:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Choncho anali kukhetsa magazi a anthu osalakwa,+

      Magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,

      Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+

      Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.+

  • Yesaya 57:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 amene mumadzutsa chilakolako chanu pakati pa mitengo ikuluikulu+ ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+ Kodi si inu amene mumapha ana m’zigwa* pakati pa matanthwe?+

  • Ezekieli 16:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “‘Unali kutenga ana ako aamuna ndi aakazi amene unandiberekera+ n’kumawapereka nsembe kwa mafano.+ Kodi zochita zako zauhulezo sizinakukwanire?

  • Ezekieli 20:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Kodi mukudziipitsa polemekeza mafano anu onse onyansa mpaka lero,+ popereka mphatso zanu mwa kuponya pamoto ana anu aamuna?+ Kodi pa nthawi imodzimodziyo ndilole kuti mufunsire kwa ine, inu anthu a nyumba ya Isiraeli?”’+

      “‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena