Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 18:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “‘Usalole kuti aliyense mwa ana ako aperekedwe+ kwa Moleki.*+ Usanyoze+ dzina la Mulungu wako mwa njira imeneyi. Ine ndine Yehova.+

  • Levitiko 20:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli, ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli, wopereka mwana wake aliyense kwa Moleki,*+ aziphedwa ndithu. Nzika za m’dziko lanu zizimupha mwa kum’ponya miyala.

  • Deuteronomo 18:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ wochita zamatsenga,+ woombeza,*+ wanyanga,+

  • 2 Mafumu 17:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Iwo anapitiriza kukana malamulo ndi pangano+ limene iye anapangana ndi makolo awo, ndiponso zikumbutso+ zimene iye anali kuwachenjeza nazo. M’malomwake anayamba kutsatira mafano opanda pake+ ndipo iwowo nawonso anakhala opanda pake.+ Anatsatira mitundu imene inawazungulira, imene Yehova anawalamula kuti asamachite zofanana nayo.+

  • Yeremiya 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kuwonjezera apo anamangira Baala+ malo okwezeka m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Anachita izi kuti azidutsitsa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto monga nsembe+ kwa Moleki.+ Ine sindinawalamule zimenezi+ ndipo sindinaganizirepo mumtima mwanga kuchita chinthu chonyansa chimenechi,+ kuti Yuda achite tchimo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena