Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 12:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Usapembedze Yehova Mulungu wako m’njira imeneyi,+ pakuti iwo amachitira milungu yawo zonse zimene zili zonyansa kwa Yehova, zimene iye amadana nazo. Pakuti iwo nthawi zonse amatentha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto monga nsembe kwa milungu yawo.+

  • 2 Mafumu 16:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Anayenda m’njira ya mafumu a ku Isiraeli,+ ndipo ngakhale mwana wake wamwamuna anamuwotcha* pamoto,+ mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa chifukwa cha ana a Isiraeli.

  • 2 Mafumu 17:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Iwo anapitiriza kuwotcha* pamoto+ ana awo aamuna ndi aakazi, kulosera+ ndi kuwombeza.*+ Anapitirizanso+ kuchita zoipa* pamaso pa Yehova ndi cholinga chomukwiyitsa.+

  • Yesaya 57:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 amene mumadzutsa chilakolako chanu pakati pa mitengo ikuluikulu+ ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+ Kodi si inu amene mumapha ana m’zigwa* pakati pa matanthwe?+

  • Yeremiya 7:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Iwo amanga malo okwezeka ku Tofeti,+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ kuti azitentha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuchita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’+

  • Ezekieli 16:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “‘Unali kutenga ana ako aamuna ndi aakazi amene unandiberekera+ n’kumawapereka nsembe kwa mafano.+ Kodi zochita zako zauhulezo sizinakukwanire?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena