Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mitembo yanu idzakhala chakudya cha cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+

  • Salimo 79:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo.+

      Matupi a okhulupirika anu awapereka kwa zilombo zakutchire.+

  • Yeremiya 7:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Mitembo ya anthu awa idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi cha zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+

  • Yeremiya 16:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+

  • Yeremiya 34:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Anthu amenewa ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa onse ofuna moyo wawo.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.+

  • Chivumbulutso 19:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 kuti mudzadye minofu+ ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu,+ ya mahatchi+ ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena