Deuteronomo 28:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mitembo yanu idzakhala chakudya cha cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+ Salimo 79:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo.+Matupi a okhulupirika anu awapereka kwa zilombo zakutchire.+ Yeremiya 12:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Cholowa changa+ chili ngati mbalame yanthenga zamitundumitundu, yodya nyama. Mbalame zodya nyama zaizungulira.+ Bwerani, sonkhanani pamodzi inu nyama zonse zam’tchire. Bwerani ndi anzanu kuti mudzaidye.+ Yeremiya 16:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+ Yeremiya 34:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Anthu amenewa ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa onse ofuna moyo wawo.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.+
26 Mitembo yanu idzakhala chakudya cha cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire, ndipo sipadzakhala woziopsa.+
2 Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo.+Matupi a okhulupirika anu awapereka kwa zilombo zakutchire.+
9 Cholowa changa+ chili ngati mbalame yanthenga zamitundumitundu, yodya nyama. Mbalame zodya nyama zaizungulira.+ Bwerani, sonkhanani pamodzi inu nyama zonse zam’tchire. Bwerani ndi anzanu kuti mudzaidye.+
4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ ndipo sadzawalira maliro+ kapena kuikidwa m’manda+ koma adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Iwo adzafa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.’+
20 Anthu amenewa ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa onse ofuna moyo wawo.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha zolengedwa zouluka m’mlengalenga ndi zilombo zakutchire.+