7 Ndidzasokoneza zolinga za Yuda ndi za Yerusalemu m’malo ano,+ ndipo ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga la adani awo komanso ndi anthu amene akufunafuna moyo wawo.+ Mitembo yawo ndidzaipereka kwa zolengedwa zouluka zam’mlengalenga ndi zilombo zakutchire kuti ikhale chakudya chawo.+