Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi+ lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafafanizidwa mwamsanga m’dziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzatalikitsa masiku anu m’dzikomo chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+

  • Deuteronomo 32:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 “Tamverani kumwamba inu, ndiloleni ndilankhule.

      Ndipo dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.+

  • Yesaya 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Imvani+ kumwamba inu, ndipo tchera khutu iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena kuti: “Ndalera ana ndi kuwakulitsa,+ koma iwo andipandukira.+

  • Yesaya 34:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Mitundu inu, bwerani pafupi kuti mumve.+ Inu mitundu ya anthu,+ mvetserani. Dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo zimvetsere.+ Nthaka ya padziko lapansi+ ndi zonse zimene zili pamenepo zimve.+

  • Yeremiya 6:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tamverani, inu okhala padziko lapansi! Ine ndikubweretsa tsoka pa anthu awa+ chifukwa cha maganizo awo,+ pakuti sanamvere mawu anga ndipo anapitirizabe kukana chilamulo changa.”+

  • Mika 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Tamverani anthu nonsenu. Mvetsera mwatcheru iwe dziko lapansi ndi anthu onse okhala mwa iwe.+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa akhale mboni yokutsutsani pa zimene mukuchita.+ Yehova akutsutseni ali m’kachisi wake woyera.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena