27 M’chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini+ mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 12, pa tsiku la 27 la mweziwo, chaka chimene Evili-merodaki+ mfumu ya Babulo anakhala mfumu, iye anakomera mtima+ Yehoyakini mfumu ya Yuda ndi kumutulutsa m’ndende.
6 Moredekai anali atatengedwa ku Yerusalemu pamodzi ndi anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+ Anthuwa ndi amene anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya+ mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anam’tenga kupita naye ku ukapolo.
37Ndiyeno Mfumu Zedekiya+ mwana wa Yosiya,+ amene Nebukadirezara mfumu ya Babulo anamuika kukhala mfumu m’dziko la Yuda,+ anayamba kulamulira m’malo mwa Koniya+ mwana wa Yehoyakimu.+