Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.

  • Deuteronomo 28:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Yehova adzakuchititsani kuti mugonje pamaso pa adani anu.+ Pokamenyana nawo nkhondo mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pawo mudzadutsa njira 7. Mudzakhala chinthu chonyansa kwa mafumu onse a dziko lapansi.+

  • 2 Mbiri 29:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Chotero mkwiyo wa Yehova+ unayakira Yuda ndi Yerusalemu, moti anawachititsa kuti akhale chinthu chonthunthumiritsa,+ chinthu chodabwitsa,+ ndiponso chinthu chochititsa anthu kuimba mluzu,+ monga momwe mukuonera ndi maso anu.

  • Yeremiya 15:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndidzawasandutsa chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho,+ chifukwa cha zimene Manase, mwana wa Hezekiya, mfumu ya Yuda, anachita mu Yerusalemu.+

  • Yeremiya 24:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndidzawatumizira lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri,+ kufikira adzatheratu m’dziko limene ndinawapatsa, iwowo ndi makolo awo.”’”+

  • Yeremiya 34:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Choncho Yehova wanena kuti, ‘Inu simunamvere mawu anga moti simunapitirize kulengeza ufulu,+ aliyense kwa m’bale wake ndi kwa mnzake. Tsopano ine ndikulengeza ufulu kwa inu,’+ watero Yehova. ‘Inu mudzafa ndi lupanga,+ mliri+ ndi njala yaikulu.+ Ndidzakusandutsani chinthu chimene maufumu onse a padziko lapansi adzanthunthumira nacho.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena