-
Mika 4:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: “Bwerani+ anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+ Iye akatiphunzitsa njira zake,+ ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.”+ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mawu a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.+
-
-
Chivumbulutso 7:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu,+ limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse,+ fuko lililonse, mtundu uliwonse,+ ndi chinenero chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu+ ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza+ m’manja mwawo.
-