Yeremiya 32:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu abwera kudzayatsa moto mzindawu kuti upseretu.+ Ayatsanso nyumba zawo chifukwa pamadenga ake amafukizirapo nsembe zautsi kwa Baala ndipo amathira nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.’+ Yeremiya 34:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 “Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikulamula ndi kubweretsanso adaniwo kumzinda uno.+ Iwo adzamenyana ndi mzindawu ndipo adzaulanda ndi kuutentha.+ Pamenepo, mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa bwinja ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.’”+ Yeremiya 38:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 “Akazi anu onse ndi ana anu aamuna akutuluka nawo panja kupita nawo kwa Akasidi, ndipo inuyo simudzapulumuka m’manja mwa Akasidiwo,+ koma dzanja la mfumu ya Babulo lidzakugwirani. Mzinda uno adzautentha chifukwa cha inu.”+ Yeremiya 39:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Akasidi anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu onse.+ Iwo anagwetsanso mpanda wa Yerusalemu.+
29 Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu abwera kudzayatsa moto mzindawu kuti upseretu.+ Ayatsanso nyumba zawo chifukwa pamadenga ake amafukizirapo nsembe zautsi kwa Baala ndipo amathira nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.’+
22 “Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikulamula ndi kubweretsanso adaniwo kumzinda uno.+ Iwo adzamenyana ndi mzindawu ndipo adzaulanda ndi kuutentha.+ Pamenepo, mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa bwinja ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.’”+
23 “Akazi anu onse ndi ana anu aamuna akutuluka nawo panja kupita nawo kwa Akasidi, ndipo inuyo simudzapulumuka m’manja mwa Akasidiwo,+ koma dzanja la mfumu ya Babulo lidzakugwirani. Mzinda uno adzautentha chifukwa cha inu.”+
8 Akasidi anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu onse.+ Iwo anagwetsanso mpanda wa Yerusalemu.+