Yeremiya 14:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Pamenepo ndinati: “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Lupanga silidzakukanthani, ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni m’malo ano.’”+ Yeremiya 23:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+ Yeremiya 27:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Anthu inu musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zonama.+ Yeremiya 28:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.+ Maliro 2:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Aneneri ako aona masomphenya achabechabe ndi opanda pake+ onena za iwe.Iwo sanaulule zolakwa zako kuti akuteteze n’cholinga choti usatengedwe kupita ku ukapolo,+Koma anali kuona masomphenya achabechabe ndi osocheretsa+ onena za iwe.
13 Pamenepo ndinati: “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Lupanga silidzakukanthani, ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni m’malo ano.’”+
17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+
14 Anthu inu musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zonama.+
14 Aneneri ako aona masomphenya achabechabe ndi opanda pake+ onena za iwe.Iwo sanaulule zolakwa zako kuti akuteteze n’cholinga choti usatengedwe kupita ku ukapolo,+Koma anali kuona masomphenya achabechabe ndi osocheretsa+ onena za iwe.