19 “‘Siliva wawo adzamuponyera mumsewu ndipo golide wawo adzaipidwa naye. Siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa m’tsiku la mkwiyo waukulu wa Yehova.+ Iwo sadzakhuta ndipo m’matumbo mwawo simudzadzaza, pakuti chumacho chakhala chowapunthwitsa ndiponso chowachititsa zolakwa.+