Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 11:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mudzi umakondwera chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,+ koma anthu oipa akawonongeka pamakhala mfuu yachisangalalo.+

  • Yesaya 44:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 “Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ pakuti Yehova wachitapo kanthu.+ Fuulani mosangalala,+ inu malo otsika kwambiri a dziko lapansi.+ Mapiri+ inu ndiponso iwe nkhalango ndi inu mitengo yonse ili mmenemo, kondwani ndi kufuula ndi chisangalalo. Pakuti Yehova wawombola Yakobo ndipo wasonyeza kukongola kwake pa Isiraeli.”+

  • Yesaya 48:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Tulukani m’Babulo anthu inu!+ Thawani m’manja mwa Akasidi.+ Nenani zimenezi ndi mfuu yachisangalalo kuti zimveke.+ Zineneni mokuwa mpaka zimveke kumalekezero a dziko lapansi.+ Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+

  • Yesaya 49:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ ndipo sangalala iwe dziko lapansi.+ Mapiri asangalale ndipo afuule ndi chisangalalo.+ Pakuti Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo amamvera chisoni anthu ake osautsidwa.+

  • Chivumbulutso 18:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Kondwerani kumwambako+ chifukwa cha zimene zamuchitikira. Inunso oyera,+ inu atumwi,+ ndi inu aneneri, kondwerani chifukwa Mulungu wamuweruza ndi kumupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani.”+

  • Chivumbulutso 19:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama* lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena