8 Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi maseche zasiya kumveka. Phokoso la anthu okondwa kwambiri silikumvekanso. Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi zeze zaleka kumveka.+
9 “Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘M’masiku anu ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi m’malo ano, inu mukuona.’+
10 Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero ndi phokoso lakusangalala m’malowo.+ Ndidzathetsanso mawu osangalala a mkwati ndi a mkwatibwi.+ Simudzamvekanso kupera kwa mphero+ ndipo simudzaonekanso kuwala kwa nyale.+
11 Pamenepo ndidzathetsa kusangalala kwake konse.+ Ndidzathetsa zikondwerero zake,+ chikondwerero cha tsiku lokhala mwezi,+ cha sabata ndi chikondwerero china chilichonse.