Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 18:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 “‘Musadzidetse ndi chilichonse cha zinthu zimenezi, chifukwa mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu yadzidetsa ndi zonse zimenezi.+

  • Numeri 35:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 “‘Musadetse dziko+ limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndiwo amadetsa dziko. Ndipo dziko lodetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe mwa njira ina, koma ndi magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+

  • Deuteronomo 21:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 mtembo wake usakhale pamtengopo usiku wonse,+ koma uzionetsetsa kuti wamuika m’manda tsiku lomwelo, chifukwa aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.+ Usaipitse nthaka yako imene Yehova Mulungu wako akukupatsa monga cholowa.+

  • Salimo 78:58
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 58 Iwo anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+

      Ndipo anamuchititsa nsanje ndi zifaniziro zawo zogoba.+

  • Salimo 106:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Choncho anali kukhetsa magazi a anthu osalakwa,+

      Magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,

      Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+

      Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.+

  • Yeremiya 16:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chotero ndisanawabwezeretse, ndidzawabwezera zolakwa zawo zonse+ ndi machimo awo onse chifukwa choipitsa dziko langa.+ Anadzaza cholowa changa ndi mitembo ya zinthu zawo zochititsa mseru ndiponso zinthu zawo zonyansazo.’”+

  • Ezekieli 36:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Iwe mwana wa munthu, pamene a nyumba ya Isiraeli anali kukhala m’dziko lawo, anali kudetsa dzikolo ndi njira zawo komanso zochita zawo.+ Pamaso panga, njira zawo zakhala ngati zonyansa za mkazi amene akusamba.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena