17Eliya+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi+ analankhula ndi Ahabu kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli+ amene ndimam’tumikira,+ sikugwa mame kapena mvula+ zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.”+
7 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ukayenda m’njira zanga ndi kusunga malamulo anga,+ udzakhala woweruza wa anthu a m’nyumba yanga+ ndipo uzidzayang’anira mabwalo a nyumba yanga. Ndithu ndidzakulola kumafika pamaso panga limodzi ndi amene aima panowa.’