Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 17:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ufa umene unali mumtsuko waukulu sunathe,+ ndipo mafuta amene anali mumtsuko waung’ono sanathe, mogwirizana ndi mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Eliya.

  • 1 Mafumu 17:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Kenako Yehova anamva mawu a Eliya,+ moti moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye, ndipo anakhala wamoyo.+

  • 1 Mafumu 18:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Pa nthawi+ yopereka nsembe yambewu, Eliya mneneri anayandikira guwa lansembelo n’kunena kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Isiraeli,+ lero zidziwike kuti inu ndinu Mulungu mu Isiraeli,+ ndi kuti ine ndine mtumiki wanu, komanso kuti ndachita zonsezi potsatira mawu anu.+

  • 1 Mafumu 18:46
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 46 Dzanja la Yehova linali ndi Eliya,+ moti iye anakokera chovala chake m’chiuno n’kuchimanga,+ ndipo anayamba kuthamanga n’kupitirira Ahabu mpaka kukafika ku Yezereeli.+

  • 2 Mafumu 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kenako Eliya anatenga chovala chake chauneneri+ n’kuchipinda. Atatero anamenya nacho madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika uku ndi uku, chotero iwo anawoloka pouma.+

  • 2 Mafumu 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pamene anali kuyenda n’kumalankhulana, anangoona galeta*+ lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi* owala ngati moto. Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo n’kuwalekanitsa, ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho n’kukwera kumwamba.+

  • 2 Mbiri 21:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Kenako anam’bweretsera kalata+ yochokera kwa mneneri Eliya.+ Kalatayo inati: “Yehova Mulungu wa Davide kholo lanu wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti sunayende m’njira za Yehosafati+ bambo ako, kapena m’njira za Asa+ mfumu ya Yuda,

  • Luka 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Komanso, adzatsogola monga kalambulabwalo wa Mulungu ali ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.+ Iye adzatembenuza mitima+ ya abambo kuti ikhale ngati ya ana, ndipo osamvera adzawatembenuzira ku nzeru yeniyeni ya anthu olungama. Adzachita izi kuti asonkhanitsire Yehova+ anthu okonzedwa.”+

  • Yohane 1:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Koma iye anati: “Iyayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena