34 Kenako anapita pabedipo ndipo anagwada n’kuweramira mwanayo.+ Anagunditsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo. Maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, manja ake anawaika pa manja a mwanayo. Anakhalabe chowerama choncho mpaka thupi la mwanayo linayamba kufunda.
44 Amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro,+ nkhope yakenso inali yomanga ndi nsalu. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “M’masuleni ndi kumuleka apite.”