Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 13:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Koma Yehova anakomera mtima+ Aisiraeli ndi kuwachitira chifundo+ ndipo anatembenukira kwa iwo chifukwa cha pangano lake+ ndi Abulahamu,+ Isaki,+ ndi Yakobo.+ Iye sanafune kuwawononga+ ndipo sanawachotse pamaso pake mpaka lero.

  • Salimo 13:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha.+

      Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu.+

  • Salimo 78:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Koma anawamvera chifundo.+ Anali kukhululukira* machimo awo+ ndipo sanali kuwawononga.+

      Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake,+

      Ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.

  • Salimo 103:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu,+

      Kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.+

  • Salimo 103:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pakuti monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,+

      Kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa.+

  • Salimo 106:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Zikatero anali kukumbukira pangano limene anachita ndi iwo,+

      Ndipo anali kuwamvera chisoni chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwake kosatha.+

  • Yeremiya 31:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, kapena mwana wanga wokondedwa?+ Pamlingo umene ndalankhula zomulanga, ndidzakumbukira kumuchitira zabwino pamlingo womwewo.+ N’chifukwa chake m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha iye.+ Mosalephera ndidzamumvera chisoni,”+ watero Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena