-
2 Samueli 24:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiyeno mngelo+ anali atatambasula dzanja lake kuloza ku Yerusalemu kuti awononge mzindawo. Pamenepo Yehova anamva chisoni+ chifukwa cha tsokalo, choncho anauza mngelo amene anali kupha anthuyo kuti: “Basi pakwanira! Tsopano tsitsa dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehova uja anali pafupi ndi malo opunthira mbewu a Arauna+ Myebusi.+
-
-
Salimo 69:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiyankheni inu Yehova, pakuti kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwabwino.+
Ndicheukireni chifukwa chifundo chanu ndi chochuluka,+
-
Yesaya 63:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+ Ndidzatamanda Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehova watichitira.+ Ndidzauza nyumba ya Isiraeli zabwino zochuluka+ zimene iye wawachitira chifukwa cha chifundo chake,+ komanso chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha ndiponso kwakukulu.
-
-
-