Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 9:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Yehova atakutumani kuchokera ku Kadesi-barinea+ kuti, ‘Kwerani ndi kukatenga dziko limene ndidzakupatsani kuti likhale lanu,’ pamenepo munapandukiranso malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ ndipo simunasonyeze chikhulupiriro+ mwa iye komanso simunamvere mawu ake.+

  • Salimo 5:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mulungu adzawapeza ndi mlandu.+

      Adzagwa ndi ziwembu zawo zomwe.+

      Muwamwaze chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zawo,+

      Chifukwa iwo akupandukirani.+

  • Salimo 107:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chifukwa anachita zinthu mopandukira+ mawu a Mulungu,+

      Ndipo ananyoza malangizo a Wam’mwambamwamba.+

  • Yesaya 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Imvani+ kumwamba inu, ndipo tchera khutu iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena kuti: “Ndalera ana ndi kuwakulitsa,+ koma iwo andipandukira.+

  • Yesaya 63:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Koma iwo anapanduka+ ndi kukhumudwitsa mzimu wake woyera.+ Chotero iye anasintha n’kukhala mdani+ wawo ndipo anachita nawo nkhondo.+

  • Ezekieli 20:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘“Koma iwo anayamba kundipandukira+ ndipo sanafune kundimvera. Aliyense wa iwo sanataye zinthu zonyansa zimene anali kuziyang’anitsitsa pozilambira ndipo sanasiye mafano onyansa a ku Iguputo.+ Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga kuti ukali wanga uthere pa iwo m’dziko la Iguputo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena