Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 5:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Davide anayamba kukhala m’malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, ndipo anawatcha Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati.

  • 2 Mbiri 26:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kuwonjezera apo Uziya anamanga nsanja+ ku Yerusalemu pafupi ndi Chipata cha Pakona,+ Chipata cha Kuchigwa,+ ndiponso pafupi ndi Mchirikizo wa Khoma, ndipo nsanjazo anazilimbitsa.

  • 2 Mbiri 32:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Kuwonjezera apo, iye analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka.+ Anamanga nsanja+ pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina.+ Anakonzanso Chimulu cha Dothi*+ cha mu Mzinda wa Davide ndipo anapanga zida+ zambiri ndi zishango.+

  • 2 Mbiri 33:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pambuyo pa zimenezi, Manase anamanga mpanda kunja+ kwa Mzinda wa Davide,+ kumadzulo kwa Gihoni,+ kuyambira m’chigwa kukafika ku Chipata cha Nsomba.+ Mpandawo unazungulira n’kukafika ku Ofeli+ ndipo unali wautali kwambiri kuchokera pansi kufika pamwamba. Kuwonjezera apo, iye anaika akuluakulu a asilikali m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+

  • Salimo 48:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Gubani mozungulira Ziyoni, anthu inu, ndipo yendayendani mmenemo,+

      Werengani nsanja zake.+

  • Maliro 4:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Mafumu a padziko lapansi ndiponso anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi,+

      Sanayembekezere kuti mdani angadzalowe pazipata za Yerusalemu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena