2 Iye wapita kukachisi ndi ku Diboni.+ Wapita kumalo okwezeka kukalira. Mowabu akulira mofuula chifukwa cha Nebo+ ndi Medeba.+ Anthu onse a mmenemo ameta mipala.+ Ndevu za munthu aliyense zametedwa.
16 Meta mpala ndi kuchotsa tsitsi lonse chifukwa cha ana ako aamuna amene unali kuwakonda.+ Meta mpala mpaka ufanane ndi wa chiwombankhanga, chifukwa chakuti ana akowo akusiya ndipo apita kudziko lina.”+