2 Iye wapita kukachisi ndi ku Diboni.+ Wapita kumalo okwezeka kukalira. Mowabu akulira mofuula chifukwa cha Nebo+ ndi Medeba.+ Anthu onse a mmenemo ameta mipala.+ Ndevu za munthu aliyense zametedwa.
29 “Meta tsitsi lako lalitalilo ndi kulitaya.+ Ukwere pamapiri opanda mitengo ndi kuimba nyimbo yoimba polira pamenepo,+ pakuti Yehova wakana+ ndi kusiya mbadwo wa anthu amene wawakwiyira.+