Yesaya
15 Uwu ndi uthenga wokhudza Mowabu:+ Chifukwa chakuti wasakazidwa usiku, Ari+ wa ku Mowabu wakhala chete. Chifukwa chakuti wasakazidwa usiku, Kiri+ wa ku Mowabu wakhala chete. 2 Iye wapita kukachisi ndi ku Diboni.+ Wapita kumalo okwezeka kukalira. Mowabu akulira mofuula chifukwa cha Nebo+ ndi Medeba.+ Anthu onse a mmenemo ameta mipala.+ Ndevu za munthu aliyense zametedwa. 3 Anthu avala ziguduli+ m’misewu yake. Pamadenga*+ ake ndi m’mabwalo a mizinda yake, aliyense akufuula. Akulira n’kumapita kumunsi.+ 4 Hesiboni ndi Eleyale+ akulira mofuula. Mawu awo amveka mpaka ku Yahazi.+ N’chifukwa chake amuna onyamula zida a ku Mowabu akungofuula. Mitima yawo ikuchita mantha kwambiri.
5 Mtima wanga ukulirira Mowabu.+ Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+ Aliyense akumakwera mtunda wa Luhiti+ akulira. Panjira yopita ku Horonaimu,+ iwo akufuula kwambiri chifukwa cha tsokalo. 6 Madzi a ku Nimurimu+ aumiratu. Msipu wauma. Udzu watha. Palibenso chobiriwira.+ 7 N’chifukwa chake akumanyamula zinthu zotsala ndi katundu amene anasunga, n’kumapita nazo kuchigwa* cha mitengo ya msondodzi. 8 Mfuu yamveka m’dziko lonse la Mowabu.+ Kufuula kwake kwamveka mpaka ku Egilaimu. Kufuula kwake kwamveka mpaka ku Beere-elimu, 9 chifukwa m’madzi onse a ku Dimoni mwadzaza magazi. Dimoni ndidzam’bweretsera zinthu zinanso, monga mikango yoti idye anthu othawa ku Mowabu ndi anthu otsala panthaka yawo.+