11 Zombo+ za Hiramu zimene zinabweretsa golide kuchokera ku Ofiri,+ zinabweretsanso matabwa a mtengo wa m’bawa+ ochuluka zedi ndi miyala yamtengo wapatali.+
21 pakuti zombo za mfumu zinkapita ku Tarisi+ limodzi ndi atumiki a Hiramu.+ Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide, siliva,+ minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko.+