Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse,+ popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. Choncho ndiwawonongera limodzi ndi dziko lapansi.+

  • 2 Mafumu 21:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+

  • Yeremiya 19:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Zidzatero chifukwa andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Iwo amaperekanso nsembe zautsi kwa milungu ina imene sanali kuidziwa,+ iwowo, makolo awo ndi mafumu a Yuda, ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+

  • Ezekieli 9:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda+ n’zazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi magazi okhetsedwa,+ ndipo mumzindamo mwadzaza zaukathyali,+ pakuti iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo m’dziko muno,+ ndipo Yehova sakuona.’+

  • Zefaniya 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Pa tsiku limenelo, ndidzalanga aliyense amene ali pafupi ndi mpando wachifumu, anthu amene adzaza nyumba za ambuye awo ndi chiwawa ndiponso chinyengo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena