Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 13:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ukadzanena mumtima mwako kuti,+ ‘N’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zandigwera?’+ pamenepo udzadziwe kuti wavulidwa siketi yako+ ndipo zidendene zako zazunzidwa chifukwa zolakwa zako zachuluka.

  • Maliro 1:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Yerusalemu wachita tchimo+ lalikulu. N’chifukwa chake wakhala chinthu chonyansa.+

      Onse amene anali kumulemekeza ayamba kumuona ngati chinthu chachabechabe,+ chifukwa aona maliseche+ ake.

      Iyenso akuusa moyo+ ndipo watembenukira kwina chifukwa cha manyazi.

  • Hoseya 2:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Tsopano ndidzamuvula kuti amuna omukonda kwambiriwo aone maliseche ake,+ ndipo palibe mwamuna amene adzamukwatula m’dzanja langa.+

  • Nahumu 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Yehova wa makamu wanena kuti: “Taona! Ine ndikukuukira,+ ndipo ndidzakuvula siketi yako ndi kukuphimba nayo kumaso moti ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ione maliseche ako+ ndi kutinso maufumu aone manyazi ako.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena