Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pamenepo iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anam’panga+ kukhala fano la mwana wa ng’ombe+ lopangidwa ndi golide wosungunula. Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+

  • Numeri 15:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 ‘Chingwecho chikhale ngati mphonje kwa inu, kuti mukachiyang’ana muzikumbukira malamulo onse+ a Yehova ndi kuwasunga. Muleke kutsatira zilakolako za mitima yanu ndi maso anu,+ chifukwa potsatira zilakolako zimenezo, mukuchita chiwerewere.+

  • Numeri 25:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Akaziwo ankabwera kudzaitana Aisiraeliwo kuti azipita nawo limodzi kokapereka nsembe kwa milungu yawo.+ Kumeneko, Aisiraeliwo ankadya ndi kugwadira milungu ya Amowabuwo.+

  • 1 Mafumu 21:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ahabu anachita zinthu zonyansa kwambiri mwa kutsatira mafano onyansa+ monga momwe Aamori, amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli, anachitira.’”+

  • Ezekieli 14:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Chotero lankhula nawo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli amene waika mtima wake pamafano ake onyansa+ ndiponso amene waika pamaso pake chinthu chopunthwitsa chimene chimamulakwitsa n’kupita kwa mneneri, ine Yehova ndidzamuyankha malinga ndi kuchuluka kwa mafano ake onyansa.+

  • Machitidwe 7:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 Chotero Mulungu anawaleka+ kuti atumikire makamu akumwamba monga mmene malemba amanenera m’buku la aneneri.+ Malembawo amati, ‘Anthu inu a nyumba ya Isiraeli, kodi m’chipululu muja munali kupereka kwa ine nyama zansembe ndi zopereka zina kwa zaka 40?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena