-
2 Mafumu 23:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Komanso guwa lansembe limene linali ku Beteli+ ndi malo okwezeka amene Yerobowamu+ mwana wa Nebati amene anachimwitsa Isiraeli+ anamanga, ngakhale guwa lansembe limenelo ndi malo okwezekawo, mfumuyo inagumula. Kenako inatentha malo okwezekawo n’kuwaperapera mpaka kusanduka fumbi. Inatenthanso mzati wopatulika.
-
-
2 Mbiri 31:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Atangomaliza kuchita zonsezi, Aisiraeli+ onse amene anali pamenepo anapita kumizinda ya Yuda+ n’kukaphwanya zipilala zopatulika,+ kukadula mizati yopatulika+ ndi kukagwetsa malo okwezeka+ ndi maguwa ansembe+ mu Yuda yense,+ mu Benjamini, mu Efuraimu+ ndi m’Manase+ mpaka kumaliza ntchitoyo. Atatero, ana onse a Isiraeli anabwerera kumizinda yawo, aliyense kumalo ake.
-
-
Hoseya 13:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Tsopano anthu ake akuchita machimo ena ndipo akugwiritsa ntchito siliva wawo popanga zifanizo zachitsulo chosungunula.+ Zifanizo zimenezo ndi mafano opangidwa mogwirizana ndi maganizo awo,+ koma zonsezi ndi ntchito za amisiri.+ Iwo amauza mafanowo kuti, ‘Amuna opereka nsembe apsompsone mafano a ana ang’ombe.’+
-