Salimo 103:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo,+Momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.+ Yesaya 38:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 M’malo mopeza mtendere ndinapeza zowawa, zowawatu zedi!+Inuyo mwamamatira moyo wanga ndipo mwauteteza kuti usapite kudzenje la chiwonongeko.+Pakuti machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.+ Yesaya 55:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+ Yeremiya 31:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 “Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena m’bale wake+ kuti, ‘Mum’dziwe Yehova!’+ pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu,”+ watero Yehova. “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.”+ Yeremiya 50:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa+ koma sichidzapezeka,” watero Yehova. “Machimo a Yuda+ adzafufuzidwa koma sadzapezeka, pakuti ine ndidzakhululukira anthu amene ndawasiya amoyo.”+
17 M’malo mopeza mtendere ndinapeza zowawa, zowawatu zedi!+Inuyo mwamamatira moyo wanga ndipo mwauteteza kuti usapite kudzenje la chiwonongeko.+Pakuti machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.+
7 Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+
34 “Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena m’bale wake+ kuti, ‘Mum’dziwe Yehova!’+ pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu,”+ watero Yehova. “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.”+
20 “M’masiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,+ cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa+ koma sichidzapezeka,” watero Yehova. “Machimo a Yuda+ adzafufuzidwa koma sadzapezeka, pakuti ine ndidzakhululukira anthu amene ndawasiya amoyo.”+