-
Yesaya 18:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 “Pa nthawi imeneyo, Yehova wa makamu+ adzapatsidwa mphatso ndi mtundu wa anthu ataliatali osalala, anthu oopedwa+ ndi mitundu yonse ya anthu. Umenewu ndi mtundu wa anthu amphamvu kwambiri, ndiponso wopambana pa nkhondo, umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje. Mphatsoyo adzaiika kuphiri la Ziyoni, kumene kuli dzina la Yehova wa makamu.”+
-
-
Aroma 15:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku kuti ndigwire ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu monga wantchito wa Khristu Yesu, wotumikira anthu a mitundu ina.+ Cholinga changa pogwira ntchito yopatulikayi+ n’chakuti mitundu ina ya anthu iperekedwe+ kwa Mulungu ngati mphatso yovomerezeka+ imene yayeretsedwa ndi mzimu woyera.+
-