Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 11:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 M’tsiku limenelo, Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri+ kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,+ ku Hamati ndi m’zilumba za m’nyanja.+

  • Yesaya 27:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Inu ana a Isiraeli, monga momwe munthu amathyolera zipatso mumtengo n’kuzisonkhanitsa+ pamodzi chimodzi ndi chimodzi, Yehova adzakusonkhanitsani inu+ amene mwamwazikana m’dera loyambira ku Mtsinje*+ mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+

  • Ezekieli 28:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndithu, iwo adzakhala m’dziko lawo+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+

  • Amosi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+

  • Mika 4:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Anthu amene anali kuyenda motsimphina ndidzawasonkhanitsanso pamodzi monga anthu otsala.+ Anthu amene anawachotsa m’dziko lawo ndi kuwapititsa kutali ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+ Yehova adzawalamulira monga mfumu m’phiri la Ziyoni kuyambira nthawi imeneyo mpaka kalekale.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena